Alimi ang’onoang’ono awalimbikitsa kugwiritsa ntchito manyowa a mbeya.

Alimi ang’onoang’ono awalimbikitsa kumagwiritsa ntchito zipangizo zopezekeratu m’madera awo ngati akufuna kuthana ndi mavuto a kuchepa kwa zokolora.

A Christopher Nkhoma, mulangizi wa mkulu wa dera la ulimi la Kapaladzala m’boma la Kasungu anena izi la chinayi pa chionetsero cha mbewu chomwe chinachitikira m’mudzi wa Kachala pansi pa dera la ulimi la Madisi ku Dowa.

A Kapaladzala ati chifukwa cha kukwera mntengo kwa zipangizo za ulimi monga feteleza alimiwa akumalephera kukolora zokwanira ndipo pakufunika kuti azikhala m’magulu osunga ndi kubwereketsa ndalama komanso kugwiritsa ntchito manyowa a Mbeya mwa zina kuti azitha kukolora zochuluka komanso kusintha moyo wawo wa chuma.

Mmodzi mwa alimiwa, a Triphonia Kachiwindi ati kudzera mu gulu lawo la Titukulane akwanitsa kusonkhanitsa ndalama zokwana MK1,585,059 pofika mwezi wa Marichi zomwe akuti zidzagwiritsidwa ntchito pogulira feteleza woti gululo lidzagawane.

“Titagula fetelezayo tinagwiritsa ntchito kupanga manyowa a mbeya omwe atithandizira kulima munda ochuluka ndipo tikuyembekeza kukolola zochuluka,” atero a Kachiwindi.

A Christopher Nkhoma, Memory Sichali komanso Arthur Kacheche, omwe ndi azilangizi a za ulimi ku Kasungu akuchita kafukufuku wa maphunziro a sukulu ya ukachenjede ya LUANAR m’mudzi wa Kachala pofuna kuona kufunika kwa kudzidalira pakati pa alimi komanso kugwiritsa ntchito manyowa ndi mbewu zamakono.

Wolemba Vincent Madalitso Chauma

Related posts

Community Radios Urged to Embrace Digitalization

Don’t View Budget with Political Lens – Expert Urge Legislators